Wolemba Ronald Ngalande
Nthenda ya Sickle Cell idakapitirirabe kukhala limodzi mwa mavuto omwe akuchulukitsa imfa za ana mdziko lino, watero unduna wa za umoyo.
Mlembi mu undunawu a Samson Mndolo ati mdziko lino mwana mmodzi mwa ana 1000 aliwonse ali ndi vuto la sickle cell ndipo anthu 9 mwa anthu 100 aliwonse atha kubereka mwana wa sickle cell.
A Mndolo anena izi pomwe dziko la Malawi lachinayi pa 19 June limakumbukira nawo tsiku loganizira za nthendayi.
Sickle cell ndi nthenda yachibadwa, otengera ku mtundu omwe amachititsa kuti magazi akhale olimba, choncho amalephera kuyenda bwino m’thupi.
Nthendayi imachititsa munthu kumva kupweteka m’thupi, kuchepa kwamagazi, kuwonongeka ziwalo ndi kuchepetsa chitetedzo cha m’thupi kumatenda ena.
Choncho undunawu ukupempha makolo ndi ena onse amene amasamalira anthu odwala nthenda ya sickle cell kuti aziwapatsa chisamaliro choyenera monga kupita nawo kuchipatala pafupipafupi.