Boma alipempha kuti liwonjezera ndalama za ku ofesi ya mkulu wozenga milandu

Wolemba Peter Davieson

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu mdziko muno la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) a Michael Kaiyatsa wapempha boma kuti liyike chidwi popereka ndalama zokwanira ku ofesi ya mkulu wozenga milandu m’boma pofuna kuti milandu monga yokupha isamatenge nthawi isanathe ku mabwalo.

Izi zayankhulidwa kutsatira ma ripoti oti anthu ankhani nkhani akusungidwa m’ndende za mdziko muno pa milandu yosiyanasiyana kuphatikizapo yakupha popanda kukawonekera kubwalo lamilandu.

A Kaiyatsa anati anthu ochuluka amakhala mndende kwa nthawi yayitali asanamve chigamulo chawo pa milandu yomwe akuwaganizira zomwe malinga ndi malamulo adziko lino ndikuwaphera ufulu anthu oganizilidwawa.

Poyankhula ndi YFM, iwo anati kuchepa kwa ndalama zomwe nthambi yoweluza milandu imapatsidwa ndi china mwa zomwe zimakoledzera kuchedwa kwa milanduyi.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *