Sindikufuna kukwaniritsa zofuna zanga — APM

Wolemba Arshavello Mponda

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Arthur Peter Mutharika (APM) omwenso ndi pulezidenti wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) ati akuyimanso pofuna kuwombola dziko lino osati kukwaniritsa zokhumba zawo.

Iwo ayankhula izi Lachisanu mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wopereka kalata zowayenereza kuzayima nawo pa chisankho cha pulezidenti cha pa 16 September.

Pa mwambowo a Mutharika analengeza kuti asankha jaji wopuma wa ku bwalo la milandu ya apilo, Justice Jane Ansah ngati wachiwiri wawo pomwe akuyima nawo pa chisankhochi.

Iwo anati asankha mayi Ansah kamba koti ndi munthu wokhwima nzeru, wa ukadaulo wa utsogoleri, okonda dziko lawo komanso owopa Mulungu.

A Mutharika anati mayi Ansah anagwira bwino ntchito ngati wapampando wa bungwe loyendetsa zisankho la MEC komanso mlangizi wa boma pa nkhani za malamulo.

Mayi Ansah, anabadwa pa 11 October mchaka cha 1955 ndipo adali mayi oyamba m’dziko muno kukhala pa udindo wa Attorney General kuchokera chaka cha 2006 mpaka 2011.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *