Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Joyce Banda (JB) omwenso ndi pulezidenti wa chipani cha People’s (PP) asankha yemwe anakhalapo wachiwiri wawo a Khumbo Kachali kuti ayime nawo limodzi pa chisankho cha pa 16 September.
A Kachali, omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Freedom, adagwirapo ntchito ndi a Banda ngati wachiwiri wawo pomwe anali mtsogoleri wa dziko lino mchaka cha 2012 mpaka 2014.
Poyankhula pambuyo popereka kalata zowayenereza kuyima nawo pa chisankhochi, a Banda anati iwo ndi a Kachali akonzeka kwa nthunthu kudzatumikila a Malawi.
Pothirirapo ndemanga pa kusankhidwa kwa a Kachali, katswiri pa nkhani za ndale a Gift Sambo adati kusankhidwanso kwa a Kachali zikusonyeza kukhulupilirana pa ndale.
A Sambo adati pa nkhani zandale pamafunika kukhulupilirana kuti mugwire bwino ntchito.
Atafunsidwa ngati Kachali ali ndikuthekera kobweretsa mavoti ndikupangitsa chipani cha PP kulowa m’boma, a Sambo adati kupambana pachisankho cha pulezidenti ndi nkhani ina yapaderadera.
Katswiri wina a Wonderful Mkhutche adali odabwa ndi kusankhidwa kwa a Kachali.
A Mkhutche adati ngakhale kuti atsogoleri awiriwa adagwirapo ntchito limodzi ngati pulezidenti wa dziko komanso wachiwiri kwa pulezidenti mchaka cha 2012 mpaka 2014 pansi pa chipani cha People’s (PP), atsogoleriwa sanamvane zochita pa ndale ndipo sanayime limodzi pa chisankho cha mchaka cha 2014.
Katswiriyu adati chiganizochi chidabwera pofuna kupeza mavoti ochuluka poyang’anira kuti mayi Banda ndi ochokera mchigawo chakum’mwera pomwe a Kachali, omwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Freedom, ndi a mchigawo chakumpoto.
A Mkhutche adatinso chiganizochi chawonetsa kuti atsogoleri awiriwa adakanamvanabe pa ndale komanso kuti mfundo za zipani zawo zokopera anthu ndi zosasiyana.