Atupele Muluzi apereka kalata ku MEC

Mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) a Atupele Muluzi loweruka adapereka kalata zawo ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC zowayenereza kupikisana nawo pa chisankho cha pa 16 September.

Pa mwambowo, a Muluzi anawonetsa kugulu Dr. Rex Kalolo omwe ayime nawo pa chisankhochi ngati wachiwiri wawo.

Dr. Kalolo ndi mwini komanso pulofeti wa mpingo wa Altar of Liberty Church of all Nations.

Mmawu awo pambuyo popereka kalata zawo, a Atupele Muluzi, anatsutsa mphekesera zoti akulowa mu mgwirizano ndi chipani cha Malawi Congress (MCP).

A Muluzi anati chipani cha UDF pakadali pano chili ndi maganizo oti chiyima pachokha koma ngati zipani zina zingagwirizane ndi maganizo awo akayendetsedwe ka dziko lino, iwo adzakhala okonzeka kuchita zokambirana za mgwirizano.

Iwo anati pamodzi ndi Dr. Kalolo, akukhulupilira za utsogoleri omwe mphamvu zimagawidwa pakati pa ma ulamuliro a boma limodzi lalikulu ndi maboma kapena zigawo zing’ono zing’ono.

A Muluzi anati ali ndi chikhulupiliro chonse kuti adzapambana.

Iwo anatinso ino ndi nthawi ya achinyamata kuti atenge ma udindo osiyanasiyana a m’dziko muno.

A Muluzi anatsindika kuti dziko la Malawi silosauka koma kuti kayendetsedwe ka dzikoli ndi komwe kali kosauka.

Pamenepa iwo anati ndiwokonzeka kusintha kayendetsedwe za zinthu mdziko muno.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *