DK ayenda ndi Mtumbuka

Wolemba Temwa Tembo

Mtsogoleri wa chipani cha UTM Dr. Dalitso Kabambe (DK) wasankha Dr. Mathews Mtumbuka ngati wachiwiri wawo pa chisankho cha pulezidenti cha pa 16 September.

Dr. Mtumbuka adachita maphunziro awo a sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi ndipo adaphunzitsapo pa sukuluyi mchaka cha 2000 mongotchulapo zochepa chabe.

Poyankhula Lamulungu mu mzinda wa Lilongwe pomwe anakasiya kalata ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) zowayenereza kudzayima nawo, a Kabambe adati ngakhale dziko la Malawi latha zaka 61 likudzilamulira palokha, ndi zomvetsa chisoni kuti pofikira pano likadali losawukitsitsa.

Iwo adati katangale, kusankhana mitundu ndinso kusatha ntchito kwa a dindo ndi zina mwa zomwe zamanga nthenje kuti dziko la Malawi lidzingokhala losawukilabe.

A Kabambe adatinso mavutowa adzakhala mbiri yakale ngati iwo angadzasankhidwe kukhala mtsogoleri wa dziko.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *