Malawi sidakhalepo ndi mtsogoleri — Chipojola

A Cosmas Felix Chipojola omwe akufuna kuyima pawokha pa chisankho cha pulezidenti pa 16 September, ati dziko lino silinakhalepo ndi mtsogoleri.

Poyankhula pambuyo popereka kalata zawo ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Loweruka, a Chpojola adati onse omwe akhala akutumikira dziko lino ndi andale osati atsogoleri.

Iwo adatsindika kuti abwera kuzatsogolera dzino lino, ndipo agonjetsa komanso sakuwopa wina aliyense.

A Chipojola adatinso ali ndikuthekera kokhazikitsa ntchito za mphanvu ya nyukiliya ku Electricity Generation Company Malawi Limited (EGENCO), motsogozedwa ndi anthu ochita bwino m’dziko muno.

Iwo adati iyi mwa zina, ndi njira imodzi yothana ndi ngongole za bungwe la International Monetary Fund (IMF) komanso kupititsa patsogolo chuma cha dziko lino.

A Chipojola adati sakuimira chifukwa chadyera koma kamba kamavuto omwe a Malawi ambiri akukumana nawo.

Iwo adachenjeza a Malawi kuti ngati sawavotera, a malawi ambiri apitilira kukumana ndizophinja zosiyanasiyana.

Pa mwambowu a Chipojola adalengeza kuti asankha a Memory Naveko ngati wachiwiri wawo yemwe akufuna kuti ayime naye limodzi.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *