Kabambe atenga kalata ya chisankho cha pulezidenti

Mtsogoleri wachipani cha UTM a Dalitso Kabambe atenga kalata yowavomereza kuzaima nawo pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino za pa 16 September.

Mkulu wofalitsa nkhani ku bungwe loyendetsa zisankho la MEC a Sangwani Mwafulirwa ati pakadali pano anthu khumi ndi mmodzi ndi omwe atenga kalatazi.

Anthuwa ndi, a Adil James Chilungo, a Joyce Banda, Dr Lazarus McCathy Chakwera, Reverend Hardwick Kaliya, a Kondwani Nankhumwa, a Atupele Austin Muluzi, a Akwame Bandawe, a Milward Tobias, a Peter Mutharika, a Frank Tumpale, ndi a Dalitso Kabambe.

About Augustine Muwotcha

View all posts by Augustine Muwotcha →

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *