Wolemba Peter Davieson
Wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo chapakati a Alfred Gangata ati achita ziwonetsero lachisanu pa 4 July mu mzinda wa Lilongwe zosakondwa ndi mchitidwe wochitira za mtopola anthu ochita ziwonetsero za bata.
Kudzera mu kalata yomwe a Gangata alembera ofesi ya bwana mkubwa wa boma la Lilongwe a Lawford Palani, iwo ati ndiwosakondwa ndi zamtopola zomwe anthu ena onyamula zikwanje adachita masiku apitawa pa ziwonetsero za mu mzinda wa Lilongwe.
Pa ziwonetserozo, anthu azikwanjewo adakhapa ndi kuvulaza omenyera ufulu wa anthu a Sylvester Namiwa.
A Gangata ati atsogolera ziwonetserozi monga mwa nzika zokhudzidwa osati ngati oyimira chipani.
Iwo ati ndi okonzeka kugwira ntchito limodzi ndi ofesi ya bwana mkubwa wa boma komanso nthambi zachitetezo powonetsetsa kuti ziwonetserezo zizachitike mwa bata.