Joyce Banda asayinira pangano loteteza amayi

Mtsogoleri wakale wa dziko lino Joyce Banda Lachitatu adasayinira pangano loteteza, kulimbikitsa ufulu wa amayi ndi atsikana komanso kuwakweza mmagawo osiyanasiyana.

Banda yemwenso ndi mtsogoleri wachipani cha People’s (PP), adasayinira panganoli ngati mbali imodzi ya zomwe adzachite ngati anthu angawasankhe kukhala mtsogoleri wa dziko lino pa chisankho cha pa 16 September, 2025.

Mtsogoleriyu adati kukweza amayi sizachilendo kwa iye kamba koti kwa zaka ziwiri zomwe anakhala mtsogoleri wadziko lino anakwanitsa kusankha amayi ambiri mmaudindo akulu akulu monga mkulu wa mabwalo amilandu wachizimayi oyamba, mlangizi wa boma pa za malamulo wachizimayi ndi ena.

Banda adatsindikanso mfundo yomwe ili mu manifesto awo yopereka maphunziro aku sekondale awulere ati pofuna kulimbikitsa maphunziro maka pakati pa atsikana omwe akukanika kutsiriza sukulu kamba ka umphawi.

Maggie Kathewera Banda, yemwe ndi mkulu wa bungwe la WOLREC komanso ndi wapampando wa Women Manifesto, anati ulendo uno akonza mfundo 15 zomwe mwazina akufuna atsogoleri apange pangano kuti adzalimbana ndi nkhanza zomwe amayi amakumana nazo, kulimbikitsa amayi pa ulimi, chuma ndi zina.

Kathewera Banda adatinso ndiwokondwa kuti manifesto ya chipani cha PP ili ndi mfundo zotukula amayi mdziko muno.

Aka ndi kachiwiri kuti mgwirizano wabungwe olimbikitsa ufulu wa amayi pansi pa women manifesto apange pangano ndi omwe akuyimila mpando wa mtsogoleri wa dziko.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *