Pofika Lamulungu, amayi asanu ndi mmodzi ndiwo anasankhidwa kukhala achiwiri kwa atsogoleri omwe akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa pulezidenti tsopano chafika pa asanu ndi mmodzi.
Izi zikutsatira kusankhidwa kwa mayi Theresa Sigele Kagona ngati wachiwiri kwa a Reverend Hardwick Kaliya omwe ayime paokha pa chisankho cha pa 16 September.
Amayi enanso omwe akuyima limodzi ndi atsogoleri oyima paokha ndi a Mervis Mwaluwuko omwe ali pambuyo pa a Adil Chilongo ndinso a Memory Naveko omwe ndi achiwiri kwa a Cosmas Felix Chipojola.
Amayi omwe akuchokera ku zipani ndi a Asiyatu Abuli omwe ndi achiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Anyamata, Atsikana, Azimayi (A.A.A), a Kwame Bandawe, a Jane Ansah achipani DPP ndinso a Bertha Ndebere achipani cha PDP.