Wolemba Arshavello Mponda
Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) labweza kalata zachisankho za a Reverend Hardwick Kaliya omwe akufuna kuyima paokha pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino pa 16 September.
Wapampando wa bungwe la MEC a Annabel Mtalimanja ati kalatazo zinalibe zowayenereza zina.
A Mtalimanja ati wachiwiri kwa a Kaliya, a Theresa Sigele Kagona sanasayinire ndinso kupereka zonse zowayenereza kuyima pa chisankho komanso sanayike chithunzi cha chiphaso cha unzika.
Iwo ati a Kaliya akakonze zolakwika zawo pasanafike pa 30 July kuti azathe kuzapikisana nawo.
Lachinayi sabata yatha, bungwe la MEC linabwezaso kalata za Dr. Daniel Dube achipani cha National patriotic (NPP) pa zifukwa ngati zomwezi.