CCTV yakhazikitsidwa kundende yaikulu ya Zomba

Nthambi yoyang’anira ndende m’dziko muno yatsimikiza kuti yakhazikitsa makamera owunika zochitika, CCTV, kundende yayikulu ya Zomba.

Mneneri wa nthambiyi, a Steve Meke, ati cholinga chake ndi kulimbikitsa chitetezo kundendeyi komanso kuthandizira ntchito yosintha khalidwe la akaidi.

Iwo ati, mwa zina, makamerawa athandiza kuthana ndi milandu yosiyanasiyana yomwe imachitika kundendezi, kuphatikizapo kulowetsa mafoni a m’manja m’nthendemo mwachinyengo.

“Ife tipitiriza kulimbikitsa chitetezo m’ndende zonse m’dziko muno komanso kuwonetsetsa kuti akaidi akamatuluka azikhala atasinthika kwathunthu,” atero a Meke.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *