Aphungu otsutsa apempha nduna ya za chuma kuti itule pansi

Aphungu am’zipani zotsutsa ku nyumba ya malamulo lolemba anapempha nduna ya za chuma a Goodall Gondwe kuti atule pansi udindo kamba kopeleka ndalama zokwana K3.4 billion zowonjezera ku madera 86 omwe anavota motsutsana ndi ma bilu azisankho.

Mtsogoleri wa chipani cha Peoples (PP) a Ralph Mhone anapempha a Gondwe kuti alongosole bwino za ndondomeko yomwe anagwiritsa ntchito posankha maderawa.

A Mhone anati izi zikusemphana ndi zomwe nyumbayo inagwirizana mu dongosolo la za chuma la mu 2017 ndi 2018.

“Aphungu omwe andunawo anawafunsa alipo 86 mwa aphungu 193 ndie ineyo ndikuti iyayi andunawa ayenera afotokoze bwino.”

Phunguyu anati siodabwa ndi nkhaniyi kamba koti ndi m’chitidwe wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) pofuna kuthokoza aphunguwa.

“Pamenepa ndichachidziwikire kuti pali ndale. Tinagwirizana kuti pakhale CDF ndi nkhani yokhudza za madzi za ndalama zokwana K35 million,” a Mhone anatero.

Poyankhura kwa atolankhani pa nkhani yomweyi, wapampando wa komiti ya nyumbayi yowona za chuma Alekeni Menyani anati nkhaniyi ndi yodandaulitsa.

“Malamulo akuti ndalama iliyonse imene yachoka m’manja mwa a Malawi singagwiritsidwe ntchito popanda nyumba ya malamulo tsono lero kodi mphamvu imeneyi ndunayi yaitenga kuti,” iwo anatero.

Poyankhapo pomwe amatsekera mtsutso pa momwe boma lagwiritsira ntchito ndalama, a Gondwe anati madera onse akuyembekezeka kulandira ndalamazi.

Iwo anati madera omwe atsala azapatsidwa ndalama zawo kudzera ku dongosolo la za chuma la chaka chino mpaka chamawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *